Pakuti gawo la Mulungu lochokera kumwamba, ndi cholowa cha Wamphamvuyonse chochokera m'mwambamo nchiyani?
Numeri 16:30 - Buku Lopatulika Koma Yehova akalenga chinthu chatsopano, ndi nthaka ikayasama pakamwa pake, nikawameza ndi zonse ali nazo, nakatsikira iwo kumanda ali ndi moyo; pamenepo mudzadziwa kuti anthu awa anyoza Mulungu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Yehova akalenga chinthu chatsopano, ndi nthaka ikayasama pakamwa pake, nikawameza ndi zonse ali nazo, nakatsikira iwo kumanda ali ndi moyo; pamenepo mudzadziwa kuti anthu awa anyoza Mulungu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma Chauta akachita chinthu china chachilendo, nthaka ikayasama ndi kuŵameza iwowo pamodzi ndi zinthu zao zonse, natsikira kumanda ali moyo, mpamene mudziŵe kuti anthu ameneŵa anyoza Chauta.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma Yehova akachita china chake chachilendo, nthaka nitsekula pakamwa pake ndi kuwameza iwo pamodzi ndi zonse zimene ali nazo, iwowa nʼkulowa mʼmanda ali moyo, pamenepo mudzazindikira kuti anthu amenewa ananyoza Yehova.” |
Pakuti gawo la Mulungu lochokera kumwamba, ndi cholowa cha Wamphamvuyonse chochokera m'mwambamo nchiyani?
Imfa iwagwere modzidzimutsa, atsikire kumanda ali amoyo, pakuti m'mokhala mwao muli zoipa pakati pao.
Pakuti Yehova adzauka monga m'phiri la Perazimu, nadzakwiya monga m'chigwa cha Gibiyoni; kuti agwire ntchito yake, ntchito yake yachilendo, ndi kuti achite chochita chake, chochita chake chachilendo.
Taonani, Ine ndidzachita chinthu chatsopano; tsopano chidzaoneka; kodi simudzachidziwa? Ndidzakonzadi njira m'chipululu, ndi mitsinje m'zidalala.
Ine ndalenga dziko lapansi, ndalengamo munthu; Ine, ngakhale manja anga, ndafunyulula kumwamba, ndi zonse za m'menemo, ndinazilamulira ndine.
Ine ndilenga kuyera ndi mdima, Ine ndilenga mtendere ndi choipa, Ine ndine Yehova wochita zinthu zonse zimenezi.
Udzayenda kwina ndi kwina masiku angati, iwe mwana wamkazi wobwerera m'mbuyo? Pakuti Yehova walenga chatsopano m'dziko lapansi: mkazi adzasanduka mphongo.
kuti mitengo iliyonse ya kumadzi isadzikuze chifukwa cha msinkhu wao, kapena kufikitsa nsonga zao pakati pa mitambo, ndi kuti amphamvu ao asaime m'kukula kwao, ndiwo onse akumwa madzi; pakuti onsewo aperekedwa kuimfa munsi mwake mwa dziko, pakati pa ana a anthu, pamodzi ndi iwo otsikira kumanda.
Chomwecho iwowa, ndi onse anali nao, anatsikira kumanda ali ndi moyo, ndi dziko linasunama pa iwo, ndipo anaonongeka pakati pa msonkhano.