Ndipo Yehova anatsika mumtambo, nanena naye, natengako mzimu uli pa iye, nauika pa akulu makumi asanu ndi awiri; ndipo kunali kuti pokhala mzimu pa iwowa, ananenera; koma osabwerezanso.
Numeri 16:25 - Buku Lopatulika Ndipo Mose anauka namuka kwa Datani ndi Abiramu; ndi akulu a Israele anamtsata. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Mose anauka namuka kwa Datani ndi Abiramu; ndi akulu a Israele anamtsata. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Mose adapita kwa Datani ndi Abiramu, ndipo akuluakulu a Aisraele adamtsatira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mose anayimirira napita kwa Datani, Abiramu ndi kwa akuluakulu a Israeli amene ankamutsatira. |
Ndipo Yehova anatsika mumtambo, nanena naye, natengako mzimu uli pa iye, nauika pa akulu makumi asanu ndi awiri; ndipo kunali kuti pokhala mzimu pa iwowa, ananenera; koma osabwerezanso.
Koma Kora, mwana wa Izihara, mwana wa Kohati, mwana wa Levi, anatenga Datani ndi Abiramu, ana a Eliyabu, ndi Oni mwana wa Peleti, ana a Rubeni;
Nena ndi khamulo, ndi kuti, Kwerani kuchoka pozungulira mahema a Kora, Datani, ndi Abiramu.
Ndipo ananena ndi khamulo, nati, Chokanitu ku mahema a anthu awa oipa, musamakhudza kanthu kao kalikonse, mungaonongeke m'zochimwa zao zonse.