Ndipo Mose anati kwa Aroni, Nena ndi khamu lonse la ana a Israele, Yandikizani pamaso pa Yehova, pakuti anamva madandaulo anu.
Numeri 16:16 - Buku Lopatulika Ndipo Mose anati kwa Kora, Iwe ndi khamu lako lonse mukhale pamaso pa Yehova mawa, iwe ndi iwowa, ndi Aroni; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Mose anati kwa Kora, Iwe ndi khamu lako lonse mukhale pamaso pa Yehova mawa, iwe ndi iwowa, ndi Aroni; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Mose adauza Kora kuti. “Maŵa iwe pamodzi ndi anthu a gulu lako 250, mubwere ku hema lamsonkhano, iweyo ndi anthu akowo ndi Aroni. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mose anati kwa Kora, “Iwe ndi okutsatira onse mudzaonekere pamaso pa Yehova mawa, iweyo ndi iwowo pamodzi ndi Aaroni. |
Ndipo Mose anati kwa Aroni, Nena ndi khamu lonse la ana a Israele, Yandikizani pamaso pa Yehova, pakuti anamva madandaulo anu.
Ndipo Yehova anati kwa Mose, ndi Aroni, ndi Miriyamu modzidzimutsa, Tulukani inu atatu kudza ku chihema chokomanako. Pamenepo anatuluka atatuwo.
Pamenepo Mose adapsa mtima, ndipo anati kwa Yehova, Musasamalira chopereka chao; sindinalande bulu wao mmodzi, kapena kuchitira choipa mmodzi wa iwowa.
nimutenge munthu yense mbale yake yofukizamo, nimuike chofukiza m'mwemo, nimubwere nazo, yense mbale yake yofukizamo pamaso pa Yehova, mbale zofukizamo mazana awiri ndi makumi asanu; ndi iwe, ndi Aroni, yense mbale yake yofukizamo.
Uwakumbutse izi, ndi kuwachitira umboni pamaso pa Ambuye, kuti asachite makani ndi mau osapindulitsa kanthu, koma ogwetsa iwo akumva.
Ndikalipo ine; chitani umboni wonditsutsa pamaso pa Yehova, ndi pamaso pa wodzozedwa wake; ndinalanda ng'ombe ya yani? Kapena ndinalanda bulu wa yani? Ndinanyenga yani? Ndinasutsa yani? Ndinalandira m'manja mwa yani chokometsera mlandu kutseka nacho maso anga? Ngati ndinatero ndidzachibwezera kwa inu.
Chifukwa chake tsono, imani pano, kuti ndiweruzane nanu pamaso pa Yehova, za ntchito zonse zolungama za Yehova anakuchitirani inu ndi makolo anu.