Numeri 16:16 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero16 Mose anati kwa Kora, “Iwe ndi okutsatira onse mudzaonekere pamaso pa Yehova mawa, iweyo ndi iwowo pamodzi ndi Aaroni. Onani mutuwoBuku Lopatulika16 Ndipo Mose anati kwa Kora, Iwe ndi khamu lako lonse mukhale pamaso pa Yehova mawa, iwe ndi iwowa, ndi Aroni; Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201416 Ndipo Mose anati kwa Kora, Iwe ndi khamu lako lonse mukhale pamaso pa Yehova mawa, iwe ndi iwowa, ndi Aroni; Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa16 Tsono Mose adauza Kora kuti. “Maŵa iwe pamodzi ndi anthu a gulu lako 250, mubwere ku hema lamsonkhano, iweyo ndi anthu akowo ndi Aroni. Onani mutuwo |
Ine ndili pano. Ngati ndinalakwa chilichonse nditsutseni pamaso pa Yehova ndi wodzozedwa wake. Kodi ndinalanda ngʼombe ya yani? Kodi ndinalanda bulu wa yani? Kodi ndani amene ndinamudyera masuku pa mutu? Kodi ndinazunza yani? Kodi ndinalandira kwa yani chiphuphu choti nʼkundidetsa mʼmaso? Ngati ndinachita chilichonse cha izi, ine ndidzakubwezerani.”