Numeri 15:6 - Buku Lopatulika Kapena ukonzere nkhosa yamphongo nsembe yaufa, awiri mwa magawo khumi a efa wa ufa wosalala, wosakaniza ndi mafuta, limodzi la magawo atatu la hini. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Kapena ukonzere nkhosa yamphongo nsembe yaufa, awiri mwa magawo khumi a efa wa ufa wosalala, wosanganiza ndi mafuta, limodzi la magawo atatu la hini. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ikakhala nkhosa yamphongo, muzipereka chopereka cha chakudya cholemera makilogaramu aŵiri, wosakaniza ndi mafuta okwanira lita limodzi ndi theka. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Pamodzi ndi nkhosa yayimuna, muzikakonzanso chopereka cha chakudya cholemera makilogalamu awiri a ufa wosalala, wosakaniza ndi mafuta okwanira lita imodzi ndi theka, |
pamenepo iye wobwera nacho chopereka chake kwa Yehova, azibwera nayo nsembe yaufa, limodzi la magawo khumi la efa wa ufa wosalala, wosakaniza ndi limodzi la magawo anai la hini la mafuta;
ndipo uzikonzera nsembe yopsereza kapena yophera, vinyo wa nsembe yothira, limodzi la magawo anai la hini, ukhale wa mwanawankhosa mmodzi.
Ndipo ubwere naye vinyo wa nsembe yothira, limodzi la magawo atatu la hini, achitire Yehova fungo lokoma.