Ndipo anafotokozera, nati Tinakafika ku dziko limene munatitumirako, ndilo ndithu moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi; ndi zipatso zake siizi.
Numeri 14:7 - Buku Lopatulika nanena ndi khamu lonse la ana a Israele, nati, Dziko tapitamo kulizonda, ndilo dziko lokometsetsa ndithu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 nanena ndi khamu lonse la ana a Israele, nati, Dziko tapitamo kulizonda, ndilo dziko lokometsetsa ndithu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo adauza mpingo wonse wa Aisraele uja kuti, “Dziko limene tidakalizondalo ndi labwino kwambiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero ndipo anati kwa gulu lonse la Aisraeli, “Dziko limene tinakayendamo ndi kuliona ndi labwino kwambiri zedi. |
Ndipo anafotokozera, nati Tinakafika ku dziko limene munatitumirako, ndilo ndithu moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi; ndi zipatso zake siizi.
Koma Kalebe anatontholetsa anthu pamaso pa Mose, nati, Tikwere ndithu ndi kulilandira lathulathu; popeza tikhozadi kuchita kumene.
Ndipo Yoswa mwana wa Nuni, ndi Kalebe mwana wa Yefune, ndiwo a iwo aja adazonda dzikolo, anang'amba zovala zao;
Ndipo anatengako zipatso za dzikoli m'manja mwao, natsikira nazo kwa ife, natibwezera mau ndi kuti, Dzikoli Yehova Mulungu wathu atipatsa ndi labwino.
Nati iwo, Taukani, tiwakwerere; pakuti tapenya dziko, ndipo taonani, ndilo lokoma ndithu; ndi inu muli chete kodi? Musamachita ulesi kumuka ndi kulowa kulandira dzikolo.