ndipo anatuluka kukomana naye Asa, nanena naye, Mundimvere, Asa, ndi onse Ayuda ndi Abenjamini, Yehova ali nanu; mukakhala ndi Iye, mukamfuna Iye, mudzampeza; koma mukamsiya, adzakusiyani.
Numeri 14:42 - Buku Lopatulika Musakwereko, pakuti Yehova sali pakati pa inu; kuti angakukantheni adani anu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Musakwereko, pakuti Yehova sali pakati pa inu; kuti angakukantheni adani anu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Musapite, kuti mungaphedwe pamaso pa adani anu, pakuti Chauta sali nanu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Musapite chifukwa Yehova sali pakati panu. Mudzagonjetsedwa ndi adani anu |
ndipo anatuluka kukomana naye Asa, nanena naye, Mundimvere, Asa, ndi onse Ayuda ndi Abenjamini, Yehova ali nanu; mukakhala ndi Iye, mukamfuna Iye, mudzampeza; koma mukamsiya, adzakusiyani.
Pakuti Aamaleke ndi Akanani ali komweko patsogolo panu, ndipo mudzagwa ndi lupanga; popeza mwabwerera m'mbuyo osatsata Yehova, chifukwa chake Yehova sadzakhala nanu.
Koma Yehova anati kwa ine, Nena nao, Musakwerako, kapena kuthira nkhondo; popeza sindili pakati panu; angakukantheni adani anu.
Pamenepo ndidzawapsera mtima tsiku ilo, ndipo ndidzawataya, ndi kuwabisira nkhope yanga, ndipo adzathedwa, ndi zoipa ndi zovuta zambiri zidzawafikira; kotero kuti adzati tsiku lija, Sizitifikira kodi zoipa izi popeza Mulungu wathu sakhala pakati pa ife?
Mwa ichi ana a Israele sangathe kuima pamaso pa adani ao, awafulatira adani ao, pakuti aperekedwa aonongeke. Sindidzakhalanso nanu mukapanda kuononga choperekedwacho, kuchichotsa pakati pa inu.
Ndipo anati, Afilisti akugwera, Samisoni. Nagalamuka iye m'tulo take, nati, Ndizituluka ngati nthawi zina, ndi kudzitakasika. Koma sanadziwe kuti Yehova adamchokera.