Koma Aamaleke ndi Akanani akhala m'chigwamo; tembenukani mawa, nimunke ulendo wanu kuchipululu, njira ya ku Nyanja Yofiira.
Numeri 14:26 - Buku Lopatulika Ndipo Yehova ananena kwa Mose ndi Aroni, nati, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yehova ananena kwa Mose ndi Aroni, nati, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta adafunsa Mose ndi Aroni kuti, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehova anawuza Mose ndi Aaroni kuti, |
Koma Aamaleke ndi Akanani akhala m'chigwamo; tembenukani mawa, nimunke ulendo wanu kuchipululu, njira ya ku Nyanja Yofiira.
Ndileke khamu loipa ili lakudandaula pa Ine kufikira liti? Ndidamva madandaulo a ana a Israele, amene amandidandaulira.
Popeza Yehova adanena za iwowa, Adzafatu m'chipululu. Ndipo sanatsalire mmodzi wa iwowa koma Kalebe mwana wa Yefune, ndi Yoswa mwana wa Nuni.