Ndipo Isibi-Benobi, ndiye wa ana a Rafa, amene kulemera kwa mkondo wake kunali masekeli mazana atatu a mkuwa, iyeyo anavala lupanga latsopano, nati aphe Davide.
Numeri 13:28 - Buku Lopatulika Komatu anthu okhala m'dzikomo ngamphamvu; ndi mizindayo nja malinga, yaikulu ndithu; ndipo tinaonakonso ana a Anaki. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Komatu anthu okhala m'dzikomo ngamphamvu; ndi midziyo nja malinga, yaikulu ndithu; ndipo tinaonakonso ana a Anaki. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Komatu anthu am'dzikomo ngamphamvu, mizinda yao ndi yozingidwa ndi malinga, ndiponso ndi yaikulu kwambiri. Kuwonjezera pamenepo, tidaonanso zidzukulu za Aanaki kumeneko. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma anthu amene amakhala mʼdzikomo ndi amphamvu, mizinda yawo ndi ya malinga aakulu kwambiri. Tinaonanso Aanaki kumeneko. |
Ndipo Isibi-Benobi, ndiye wa ana a Rafa, amene kulemera kwa mkondo wake kunali masekeli mazana atatu a mkuwa, iyeyo anavala lupanga latsopano, nati aphe Davide.
Tinaonakonso Anefili, ana a Anaki, obadwa ndi Anefili; ndipo tinaoneka m'maso mwathu ngati ziwala; momwemonso tinaoneka m'maso mwao.
Tikwere kuti? Abale athu atimyukitsa mitima yathu, ndi kuti, Anthuwo ndiwo aakulu ndi aatali akuposa ife; mizinda ndi yaikulu ndi ya malinga ofikira m'mwamba: tinaonakonso ana a Anaki.
ndiwo anthu aakulu, ndi ambiri, ndi ataliatali, monga Aanaki; koma Yehova anawaononga pamaso pao; ndipo analanda dziko lao, nakhala m'malo mwao;
Yonseyi ndiyo mizinda yozinga ndi malinga aatali, zitseko, ndi mipiringidzo; pamodzi ndi midzi yambirimbiri yopanda malinga.
Panalibe Aanaki otsala m'dziko la ana a Israele; koma mu Gaza ndi mu Gati ndi mu Asidodi anatsalamo ena.
Ndipo tsopano, ndipatseni phiri ili limene Yehova ananenera tsiku lija; pakuti udamva tsiku lijalo kuti Aanaki anali komweko, ndi mizinda yaikulu ndi yamalinga; kapena Yehova adzakhala ndi ine, kuti ndiwaingitse monga ananena Yehova.
Ndipo Kalebe anaingitsako ana aamuna atatu a Anaki, ndiwo Sesai, ndi Ahimani, ndi Talimai, ana a Anaki.
Ndipo anapatsa Kalebe Hebroni monga Mose adanena; iye nawaingitsa komweko ana aamuna atatu a Anaki.