Ndipo Mose analowa m'kati mwa mtambo, nakwera m'phirimo; ndipo Mose anakhala m'phiri masiku makumi anai usana ndi usiku.
Numeri 13:25 - Buku Lopatulika Pamenepo anabwerera atazonda dziko, atatha masiku makumi anai. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo anabwerera atazonda dziko, atatha masiku makumi anai. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Patapita masiku makumi anai, anthu aja adabwerako kumene adakazonda dziko kuja. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Patapita masiku makumi anayi, anthu aja anabwerako kokazonda dziko lija. |
Ndipo Mose analowa m'kati mwa mtambo, nakwera m'phirimo; ndipo Mose anakhala m'phiri masiku makumi anai usana ndi usiku.
Ndipo anakhala pomwepo ndi Yehova masiku makumi anai, usana ndi usiku; sanadye mkate kapena kumwa madzi. Ndipo analembera pa magomewo mau a panganolo, mau khumiwo.
Ndipo anamuka, nadza kwa Mose, ndi Aroni, ndi khamu lonse la ana a Israele, ku chipululu cha Parani ku Kadesi; ndipo anabwezera mau iwowa, ndi khamu lonse, nawaonetsa zipatso za dzikoli.