Koma iwe, dzisankhire mwa anthu ako onse, amuna anzeru, akuopa Mulungu, amuna oona, akudana nalo phindu la chinyengo; nuwaikire iwo oterewa, akulu a pa zikwi, akulu a pa mazana, akulu a pa makumi asanu, akulu a pa makumi;
Numeri 10:4 - Buku Lopatulika Akaliza limodzi, pamenepo akalonga, akulu a zikwi a mu Israele, azisonkhana kuli iwe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Akaliza limodzi, pamenepo akalonga, akulu a zikwi a m'Israele, azisonkhana kuli iwe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma akangoliza limodzi lokha, atsogoleri a mafuko a Aisraele ndiwo asonkhane kwa iwe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Akaliza limodzi lokha, atsogoleri, akulu a mafuko a Aisraeli, asonkhane kwa iwe. |
Koma iwe, dzisankhire mwa anthu ako onse, amuna anzeru, akuopa Mulungu, amuna oona, akudana nalo phindu la chinyengo; nuwaikire iwo oterewa, akulu a pa zikwi, akulu a pa mazana, akulu a pa makumi asanu, akulu a pa makumi;
akalonga a Israele, akulu a nyumba za makolo ao, anapereka nsembe, ndiwo akalonga a mafuko akuyang'anira owerengedwa;
Potero ndinatenga akulu a mafuko anu, amuna anzeru, ndi odziwika, ndi kuwaika akhale akulu anu, atsogoleri a zikwi, ndi atsogoleri a mazana, ndi atsogoleri a makumi asanu, ndi atsogoleri a makumi, ndi akapitao, a mafuko anu.