Ndipo anamdalitsa Rebeka, nati kwa iye, Mlongo wathu ndiwe, iwe ukhale amai wa anthu zikwizikwi, mbeu zako zigonjetse chipata cha iwo akudana nao.
Numeri 10:36 - Buku Lopatulika Ndi pakupumula ili anati, Bwerani Yehova kwa zikwizikwi za Israele. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndi pakupumula ili anati, Bwerani Yehova kwa zikwizikwi za Israele. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mtambowo ukaima, Mose ankati, “Inu Chauta, bwererani kwa Aisraele anu amene ali zikwi zosaŵerengeka.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Pamene likupumula, ankanena kuti, “Bwererani, Inu Yehova, ku chinamtindi cha Aisraeli.” |
Ndipo anamdalitsa Rebeka, nati kwa iye, Mlongo wathu ndiwe, iwe ukhale amai wa anthu zikwizikwi, mbeu zako zigonjetse chipata cha iwo akudana nao.
Yehova bwanji mwatisocheretsa kusiya njira zanu, ndi kuumitsa mitima yathu tisakuopeni? Bwerani, chifukwa cha atumiki anu, mafuko a cholowa chanu.
Yehova Mulungu wanu anakuchulukitsani, ndipo taonani, lero muchuluka ngati nyenyezi za kumwamba.