Numeri 10:31 - Buku Lopatulika Koma anati, Usatisiyetu; popeza udziwa poyenera kumanga ife m'chipululu, ndipo udzakhala maso athu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma anati, Usatisiyetu; popeza udziwa poyenera kumanga ife m'chipululu, ndipo udzakhala maso athu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo Mose adati, “Musatisiye, ndapota nanu, poti inu mukudziŵa kumene tingamange mahema m'chipululu muno, ndipo mudzakhala maso athu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Mose anati, “Pepa usatisiye popeza ukudziwa kumene tingamange misasa mʼchipululu muno ndipo udzakhala maso athu. |
Ine ndidzakulangiza ndi kuphunzitsa iwe za njira ukayendayo; ndidzakupangira ndi diso langa lakuyang'ana iwe.
Ndipo kudzatero, ukamuka nafe, inde, kudzali kuti zokoma zilizonse Yehova atichitira ife, zomwezo tidzakuchitira iwe.