Ndipo Leya anati, Mulungu wandipatsa ine mphotho yanga, chifukwa ndapatsa mdzakazi wanga kwa mwamuna wanga: namutcha dzina lake Isakara.
Numeri 1:28 - Buku Lopatulika A ana a Isakara, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 A ana a Isakara, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mwa zidzukulu za Isakara adalemba maina a amuna onse otha kumenya nkhondo, a zaka 20 ndi a zaka zopitirirapo, potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kuchokera mwa zidzukulu za Isakara: Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo. |
Ndipo Leya anati, Mulungu wandipatsa ine mphotho yanga, chifukwa ndapatsa mdzakazi wanga kwa mwamuna wanga: namutcha dzina lake Isakara.
owerengedwa ao a fuko la Yuda, ndiwo zikwi makumi asanu ndi awiri mphambu zinai kudza mazana asanu ndi limodzi.
owerengedwa ao a fuko la Isakara, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zinai kudza mazana anai.