A ana a Gadi, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;
Numeri 1:25 - Buku Lopatulika owerengedwa ao a fuko la Gadi, ndiwo zikwi makumi anai mphambu zisanu kudza mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 owerengedwa ao a fuko la Gadi, ndiwo zikwi makumi anai mphambu zisanu kudza mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono ataŵerenga maina onse a m'fuko la Gadi, adapezeka kuti ali 45,650. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Gadi chinali 45, 650. |
A ana a Gadi, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;
A ana a Yuda, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;
Ndi khamu lake, ndi owerengedwa ake, ndiwo zikwi makumi anai mphambu zisanu kudza mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu.
Iwo ndiwo mabanja a ana a Gadi, monga mwa owerengedwa ao, zikwi makumi anai ndi mazana asanu.