Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Nehemiya 9:9 - Buku Lopatulika

Ndipo munapenya msauko wa makolo athu mu Ejipito, nimunamva kufuula kwao ku Nyanja Yofiira,

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo munapenya msauko wa makolo athu m'Ejipito, nimunamva kufuula kwao ku Nyanja Yofiira,

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

“Mudaona kuzunzika kwa makolo athu ku Ejipito kuja, ndipo mudamva kulira kwao ku Nyanja Yofiira.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

“Munaona kuzunzika kwa makolo athu ku Igupto. Munamva kufuwula kwawo pa Nyanja Yofiira.

Onani mutuwo



Nehemiya 9:9
8 Mawu Ofanana  

Ndipo Israele anaiona ntchito yaikulu imene Yehova anachitira Aejipito, ndipo anthuwo anaopa Yehova; nakhulupirira Yehova ndi mtumiki wake Mose.


Ndipo Mulungu anapenya Aisraele, ndi Mulungu anadziwa.


Muka, nukasonkhanitse akulu a Israele, nunene nao, Yehova, Mulungu wa makolo anu anandionekera ine, Mulungu wa Abrahamu, Isaki ndi Yakobo, ndi kuti, Ndakuzondani ndithu, ndi kuona chomwe akuchitirani mu Ejipito;


tsiku lomwelo ndinawakwezera dzanja langa kuwatulutsa m'dziko la Ejipito, kunka nao kudziko ndinawazondera, moyenda mkaka ndi uchi, ndilo lokometsetsa mwa maiko onse;


Kuona ndaona choipidwa nacho anthu anga ali mu Ejipito, ndipo amva kubuula kwao; ndipo ndatsika kuwalanditsa; ndipo tsopano, tiye kuno, ndikutume ku Ejipito.


Ndipo mtundu umene udzawayesa akapolo, ndidzauweruza Ine, anatero Mulungu; ndipo zitapita izi adzatuluka, nadzanditumikira Ine m'malo muno.