Nehemiya 9:10 - Buku Lopatulika10 nimunachitira zizindikiro ndi zodabwitsa Farao ndi akapolo ake onse, ndi anthu onse a m'dziko lake; popeza munadziwa kuti anawachitira modzikuza; ndipo munadzibukitsira dzina monga lero lino. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201410 nimunachitira zizindikiro ndi zodabwitsa Farao ndi akapolo ake onse, ndi anthu onse a m'dziko lake; popeza munadziwa kuti anawachitira modzikuza; ndipo munadzibukitsira dzina monga lero lino. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa10 Mudachita zizindikiro ndi zodabwitsa pamaso pa Farao, antchito ake onse, ndi anthu onse okhala m'dziko mwake, popeza kuti mudaadziŵa kuti iwowo adazunza makolo athu. Nchifukwa chake mbiri yanu idakula monga momwe iliri mpaka lero lino. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero10 Inu munachita zizindikiro zozizwitsa ndi zodabwitsa kutsutsana ndi Farao, pamaso pa Farao, nduna zake ndi anthu onse a mʼdziko lake, pakuti Inu munadziwa kuti anazunza makolo athu. Inu munadzipangira nokha dzina, monga zilili mpaka lero lino. Onani mutuwo |
koma munadzikweza kutsutsana naye Ambuye wa Kumwamba; ndipo anabwera nazo zotengera za nyumba yake kwa inu; ndi inu ndi akulu anu, akazi anu ndi akazi anu aang'ono, mwamweramo vinyo; mwalemekezanso milungu yasiliva, ndi yagolide, yamkuwa, yachitsulo, yamtengo, ndi yamwala, imene siiona kapena kumva, kapena kudziwa; ndi Mulungu amene m'dzanja mwake muli mpweya wanu, ndi njira zanu zonse, yemweyo simunamchitire ulemu.