napereka ku utumiki wa nyumba ya Mulungu golide matalente zikwi zisanu, ndi madariki zikwi khumi; ndi siliva matalente zikwi khumi, ndi mkuwa matalente zikwi khumi mphambu zisanu ndi zitatu, ndi chitsulo matalente zikwi zana limodzi.
Nehemiya 7:71 - Buku Lopatulika Enanso a akulu a nyumba za makolo anapereka kuchuma cha ntchitoyi, madariki agolide zikwi makumi awiri, ndi miyeso ya siliva zikwi ziwiri mphambu mazana awiri. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Enanso a akulu a nyumba za makolo anapereka kuchuma cha ntchitoyi, madariki agolide zikwi makumi awiri, ndi miyeso ya mina ya siliva zikwi ziwiri mphambu mazana awiri. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Atsogoleri ena a mabanja adapereka mosungira chumamo ndalama zagolide za makilogaramu 168, ndiponso ndalama zasiliva za makilogaramu 1,250. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Atsogoleri ena amabanja anapereka ku thumba losungira chuma ndalama zagolide zokwana makilogalamu 168, ndiponso ndalama za siliva zokwana makilogalamu 1,250. |
napereka ku utumiki wa nyumba ya Mulungu golide matalente zikwi zisanu, ndi madariki zikwi khumi; ndi siliva matalente zikwi khumi, ndi mkuwa matalente zikwi khumi mphambu zisanu ndi zitatu, ndi chitsulo matalente zikwi zana limodzi.
Ndipo ena a akulu a nyumba za makolo anapereka kuntchito. Kazembeyo anapereka kuchuma madariki agolide chikwi chimodzi, mbale zowazira makumi asanu, malaya a ansembe makumi atatu.
Zopereka za anthu otsala ndizo madariki agolide zikwi makumi awiri, ndi miyeso ya siliva zikwi ziwiri, ndi malaya a ansembe makumi asanu ndi limodzi mphambu asanu ndi awiri.
Nanga kwa Iye wosasamalira nkhope za akalonga, wosasiyanitsa pakati pa wolemera ndi wosauka? Pakuti onsewo ndiwo ntchito ya manja ake.
Pakuti ngati chivomerezocho chili pomwepo, munthu alandiridwa monga momwe ali nacho, si monga chimsowa.