Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 7:70 - Buku Lopatulika

70 Ndipo ena a akulu a nyumba za makolo anapereka kuntchito. Kazembeyo anapereka kuchuma madariki agolide chikwi chimodzi, mbale zowazira makumi asanu, malaya a ansembe makumi atatu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

70 Ndipo ena a akulu a nyumba za makolo anapereka kuntchito. Kazembeyo anapereka kuchuma madariki agolide chikwi chimodzi, mbale zowazira makumi asanu, malaya a ansembe makumi atatu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

70 Atsogoleri ena a mabanja adapereka mphatso zothandizira ntchito. Bwanamkubwa adapereka ku thumba la chuma ndalama zagolide za makilogaramu asanu ndi atatu, mbale makumi asanu, ndiponso mikanjo ya ansembe yokwanira 530.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

70 Atsogoleri ena a mabanja anapereka mphatso zothandizira ntchito. Bwanamkubwa anapereka ku thumba losungira chuma, ndalama zagolide za makilogalamu asanu ndi atatu, mabeseni makumi asanu ndi zovala za ansembe 530.

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 7:70
15 Mawu Ofanana  

ndi miphikayo, ndi zoolerazo, ndi mbalezo; inde zotengera zonse zimene Hiramu anampangira mfumu Solomoni za m'nyumba ya Yehova, zinali za mkuwa wonyezimira.


ndi mitengo, ndi mbale zowazira, ndi zikho za golide woona, ndi cha mitsuko yake yagolide, woyesedwa kulemera kwake mtsuko uliwonse; ndi cha mitsuko yasiliva woyesedwa kulemera kwake mtsuko uliwonse;


Ndipo Huramu anapanga miphika, ndi zoolera zake, ndi mbale zowazira zake. Natsiriza Huramu ntchito adaichitira mfumu Solomoni m'nyumba ya Mulungu:


Anapanganso magome khumi, nawaika mu Kachisi, asanu ku dzanja lamanja, ndi asanu ku dzanja lamanzere. Napanga mbale zowazira zana limodzi zagolide.


Okhomera chizindikiro tsono ndiwo Nehemiya, Tirisata mwana wa Hakaliya, ndi Zedekiya,


Ndipo kazembe anawauza kuti asadyeko zopatulika kwambiri, mpaka wauka wansembe wokhala ndi Urimu ndi Tumimu.


ngamira zao mazana anai mphambu makumi atatu kudza asanu; abulu ao zikwi zisanu ndi chimodzi mphambu mazana asanu ndi awiri kudza makumi awiri.


Enanso a akulu a nyumba za makolo anapereka kuchuma cha ntchitoyi, madariki agolide zikwi makumi awiri, ndi miyeso ya siliva zikwi ziwiri mphambu mazana awiri.


Ndipo Nehemiya, ndiye kazembe, ndi Ezara wansembe mlembiyo, ndi Alevi ophunzitsa anthu, ananena ndi anthu onse, Lero ndilo lopatulikira Yehova Mulungu wanu, musamachita maliro, musamalira misozi. Popeza anthu onse analira misozi pakumva mau a chilamulo.


Ndipo muzitenga mpukutu wa hisope, ndi kuuviika m'mwazi uli m'mbale, ndi kupaka mwazi uli m'mbalemo pa mphuthu ya pamwamba ndi pambali; koma inu, asatuluke munthu pakhomo pa nyumba yake kufikira m'mawa.


Ndipo Mose anagawa mwaziwo, nathira wina m'zotengera, nawaza wina paguwa la nsembe


Ndi zikho, ndi zopalira moto, ndi mbale, ndi miphika, ndi zoikaponyali, ndi zipande, ndi mitsuko; ndi golide, wa zija zagolide, ndi siliva, wa zija zasiliva, kapitao wa alonda anazichotsa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa