Ndipo mfumu inaitana Agibiyoni, ninena nao (koma Agibiyoni, sanali a ana a Israele, koma a Aamori otsala; ndipo ana a Israele anawalumbirira kwa iwo, koma Saulo anafuna kuwapha mwa changu chake cha kwa ana a Israele ndi a Yuda).
Nehemiya 3:7 - Buku Lopatulika Ndi pambali pao anakonza Melatiya Mgibeoni, ndi Yadoni Mmeronoti, ndi amuna a ku Gibiyoni, ndi a ku Mizipa, wa ulamuliro wa chiwanga tsidya lino la mtsinje. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndi pambali pao anakonza Melatiya Mgibeoni, ndi Yadoni Mmeronoti, ndi amuna a ku Gibiyoni, ndi a ku Mizipa, wa ulamuliro wa chiwanga tsidya lino la mtsinje. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pambali pa iwowo, Melatiya Mgibiyoni ndi Yadoni Mmeronoti, ndiponso anthu a ku Gibiyoni ndi a ku Mizipa, adakonza chigawo chao mpaka ku nyumba ya bwanamkubwa wa chigawo cha Patsidya pa Yufurate. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pambali pawo Melatiya Mgibeyoni ndi Yadoni Mmerenoti ndiponso anthu a ku Gibiyoni ndi a ku Mizipa anakonza chigawo chawo mpaka ku nyumba ya bwanamkubwa wa chigawo cha Patsidya pa Yufurate. |
Ndipo mfumu inaitana Agibiyoni, ninena nao (koma Agibiyoni, sanali a ana a Israele, koma a Aamori otsala; ndipo ana a Israele anawalumbirira kwa iwo, koma Saulo anafuna kuwapha mwa changu chake cha kwa ana a Israele ndi a Yuda).
ndi woyang'anira ngamira ndiye Obili Mwismaele; ndi woyang'anira abulu ndiye Yedeiya Mmeronoti;
Pamenepo Asa mfumu anatenga Ayuda onse, ndipo anatuta miyala ya ku Rama, ndi mitengo yake, imene Baasa adamanga nayo, namangira Geba ndi Mizipa.
Zolembedwa m'kalatayo anazitumiza kwa Arita-kisereksesi mfumu: ife akapolo anu, anthu a tsidya lino la mtsinjewo, tikupatsani moni.
Ndi pa mbali pake Ezere mwana wa Yesuwa, mkulu wa Mizipa, anakonza gawo lina, pandunji pokwerera kunyumba yosungamo zida za nkhondo, popindirira linga.