Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 3:19 - Buku Lopatulika

19 Ndi pa mbali pake Ezere mwana wa Yesuwa, mkulu wa Mizipa, anakonza gawo lina, pandunji pokwerera kunyumba yosungamo zida za nkhondo, popindirira linga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Ndi pa mbali pake Ezere mwana wa Yesuwa, mkulu wa Mizipa, anakonza gawo lina, pandunji pokwerera kunyumba yosungamo zida za nkhondo, popindirira linga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Pambali pa iyeyo Ezere mwana wa Yesuwa wolamulira Mizipa, adakonza chigawo china choyang'anana ndi chikweza chofikira ku malo osungira zida zankhondo pa Ndonyo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Motsatana naye Ezeri mwana wa Yesuwa, wolamulira Mizipa anakonza chigawo chinanso choyangʼanana ndi chikweza chofikira ku nyumba yosungira zida za nkhondo pa ngodya.

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 3:19
6 Mawu Ofanana  

Uziya anamanganso nsanja mu Yerusalemu pa Chipata cha Kungodya, ndi pa Chipata cha ku Chigwa, ndi popindika linga; nazilimbikitsa.


Ndi Alevi ndiwo Yesuwa mwana wa Azaniya, Binuyi wa ana a Henadadi, Kadimiyele;


Ndi Alevi ndiwo Yesuwa, Binuyi, Kadimiyele, Serebiya, Yuda, ndi Mataniya; iye ndi abale ake amatsogolera mayamiko.


Ndi Chipata cha ku Kasupe anachikonza Salumu mwana wa Kolihoze mkulu wa dziko la Mizipa anachimanga, nachikomaniza pamwamba pake, naika zitseko zake, zokowera zake, ndi mipiringidzo yake; ndiponso linga la dziwe la Sela pamunda wa mfumu, ndi kufikira kumakwerero otsikira kumzinda wa Davide.


Potsatizana naye anakonza abale ao, Bavai mwana wa Henadadi, mkulu wa dera lina la dziko la Keila.


Potsatizana naye Binuyi mwana wa Henadadi anakonza gawo lina, kuyambira kunyumba ya Azariya kufikira popindirira kufikira kungodya.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa