Mateyu 8:7 - Buku Lopatulika Ndipo Yesu ananena naye, Ndifika Ine, ndidzamchiritsa iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yesu ananena naye, Ndifika Ine, ndidzamchiritsa iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu adamuuza kuti, “Chabwino, ndibwera kudzamchiritsa.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Yesu anati kwa iye, “Ine ndibwera kudzamuchiritsa.” |
Koma kenturiyoyo anavomera nati, Ambuye, sindiyenera kuti mukalowe pansi pa tsindwi langa iai; koma mungonena mau, ndipo adzachiritsidwa mnyamata wanga.
Ndipo Yesu anapita nao. Ndipo pakufika Iye tsono pafupi pa nyumba yake, kenturiyo anatuma kwa Iye abwenzi ake, kunena naye, Ambuye, musadzivute; pakuti sindiyenera ine kuti mudzalowe pansi pa tsindwi langa;