Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 8:8 - Buku Lopatulika

8 Koma kenturiyoyo anavomera nati, Ambuye, sindiyenera kuti mukalowe pansi pa tsindwi langa iai; koma mungonena mau, ndipo adzachiritsidwa mnyamata wanga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Koma kenturiyoyo anavomera nati, Ambuye, sindiyenera kuti mukalowe pansi pa chindwi langa iai; koma mungonena mau, ndipo adzachiritsidwa mnyamata wanga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Koma mkulu uja adati, “Ambuye, sindili woyenera kuti Inu nkuloŵa m'nyumba mwanga. Mungonena mau okha, ndipo wantchito wangayo achira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Kenturiyo uja anayankha kuti, “Ambuye, ndine wosayenera kuti Inu mukalowe mʼnyumba mwanga. Koma mungonena mawu ndipo wantchito wanga adzachiritsidwa.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 8:8
18 Mawu Ofanana  

sindiyenera zazing'ono za zifundo zonse, ndi zoona zonse, zimene mwamchitira kapolo wanu: chifukwa ndindodo yanga ndinaoloka pa Yordani uyu; ndipo tsopano ndili makamu awiri.


Yehova, mwamva chikhumbo cha ozunzika, mudzakhazikitsa mtima wao, mudzatchereza khutu lanu;


Atumiza mau ake nawachiritsa, nawapulumutsa ku chionongeko chao.


Pakuti ananena, ndipo chinachitidwa; analamulira, ndipo chinakhazikika.


Tenga ndodoyo, nusonkhanitse khamulo; iwe ndi Aroni mbale wako, munene ndi thanthwe pamaso pao, kuti liwapatse madzi; potero uwatulutsire madzi m'thanthwe, ndi kumwetsa khamu la anthu ndi zoweta zao.


Inetu ndikubatizani inu ndi madzi kuloza ku kutembenuka mtima; koma Iye wakudza pambuyo panga, ali wakundiposa mphamvu, amene sindiyenera kunyamula nsapato zake: Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto:


Koma Yohane anati amkanize, nanena, Ndiyenera ine kubatizidwa ndi Inu, ndipo Inu mudza kwa ine kodi?


Ndipo Yesu anatambalitsa dzanja lake, namkhudza iye, nati, Ndifuna; takonzedwa. Ndipo pomwepo khate lake linachoka.


Ndipo Yesu ananena naye, Ndifika Ine, ndidzamchiritsa iye.


Pakuti inenso ndili munthu wakumvera ulamuliro, ndili nao asilikali akundimvera ine: ndipo ndinena kwa uyu, Muka, namuka; ndi kwa wina, Idza, nadza; ndi kwa kapolo wanga, Chita ichi, nachita.


sindiyeneranso konse kutchulidwa mwana wanu; mundiyese ine ngati mmodzi wa antchito anu.


Ndipo mwanayo anati kwa iye, Atate ndinachimwira Kumwamba ndi pamaso panu, sindiyeneranso konse kutchulidwa mwana wanu.


Koma Simoni Petro, pamene anaona, anagwa pansi pa mawondo ake a Yesu, nanena, Muchoke kwa ine, Ambuye, chifukwa ndine munthu wochimwa.


ndiye wakudza pambuyo panga, amene sindiyenera kummasulira chingwe cha nsapato yake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa