pamene anaonetsa zolemera za ufumu wake waulemu, ndi ulemerero wa ukulu wake woposa, masiku ambiri, ndiwo masiku zana limodzi mphambu makumi asanu ndi atatu.
Mateyu 4:8 - Buku Lopatulika Pomwepo mdierekezi anamuka naye kuphiri lalitali, namuonetsa maufumu onse a dziko lapansi, ndi ulemerero wao; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pomwepo mdierekezi anamuka naye kuphiri lalitali, namuonetsa maufumu onse a dziko lapansi, ndi ulemerero wao; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Potsiriza Satana adatenga Yesu kupita naye pa phiri lalitali kwambiri, ndipo adamuwonetsa maufumu onse a pansi pano ndi ulemerero wake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka mdierekezi anamutengera Yesu ku phiri lalitali kwambiri namuonetsa maufumu onse a dziko lapansi ndi ulemerero wawo. |
pamene anaonetsa zolemera za ufumu wake waulemu, ndi ulemerero wa ukulu wake woposa, masiku ambiri, ndiwo masiku zana limodzi mphambu makumi asanu ndi atatu.
Nawawerengera Hamani kulemera kwake kwakukulu, ndi ana ake ochuluka, ndi zonse mfumu idamkuza nazo, ndi umo adamkweza koposa akalonga ndi anyamata a mfumu.
Mfumu inanena, niti, Suyu Babiloni wamkulu ndinammanga, akhale pokhala pachifumu, ndi mphamvu yanga yaikulu uoneke ulemerero wachifumu wanga?
Ndipo Balamu anati kwa Balaki, Imani pa nsembe yopsereza yanu, ndipite ine, kapena Yehova akadza kukomana ndi ine; ndipo chimene akandionetsa ine ndidzakufotokozerani. Ndipo anapita pamsanje poyera.
Pakuti munthu adzapindulanji, akalandira dziko lonse, nataya moyo wake? Kapena munthu adzaperekanji chosintha ndi moyo wake?
Pamenepo mdierekezi anamuka naye kumzinda woyera; namuika Iye pamwamba penipeni pa Kachisi,
Pakuti Atate akonda Mwana, namuonetsa zonse azichita yekha: ndipo adzamuonetsa ntchito zoposa izi, kuti mukazizwe.
Popeza, Anthu onse akunga udzu, ndi ulemerero wao wonse ngati duwa la udzu. Udzuwo ungofota, ndi duwa lake lingogwa;
Ndipo mngelo wachisanu ndi chiwiri anaomba lipenga, ndipo panakhala mau aakulu mu Mwamba, ndi kunena, Ufumu wa dziko lapansi wayamba kukhala wa Ambuye wathu, ndi wa Khristu wake: ndipo adzachita ufumu kufikira nthawi za nthawi.