Chifukwa chake tsopano konzani njira zanu ndi machitidwe anu, ndi kumvera mau a Yehova Mulungu wanu; ndipo Yehova adzaleka choipa chimene ananenera inu.
Mateyu 3:8 - Buku Lopatulika Onetsani inu zipatso zakuyenera kutembenuka mtima: Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Onetsani inu zipatso zakuyenera kutembenuka mtima: Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chitanitu ntchito zosonyeza kuti mwatembenukadi mtima. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Onetsani chipatso cha kutembenuka mtima. |
Chifukwa chake tsopano konzani njira zanu ndi machitidwe anu, ndi kumvera mau a Yehova Mulungu wanu; ndipo Yehova adzaleka choipa chimene ananenera inu.
Kapena nyumba ya Yuda idzamva choipa chonse chimene nditi ndidzawachitire; kuti abwerere yense kuleka njira yake yoipa; kuti ndikhululukire mphulupulu yao ndi tchimo lao.
Popeza Yohane anadza kwa inu m'njira ya chilungamo, ndipo simunamvere iye; koma amisonkho ndi akazi achiwerewere anammvera iye; ndipo inu, m'mene munachiona, simunalape pambuyo pake, kuti mumvere iye.
Chifukwa chake balani zipatso zakuyenera kulapa mtima, ndipo musayambe kunena mwa inu nokha, Atate wathu tili naye ndiye Abrahamu: pakuti ndinena kwa inu, kuti ali ndi mphamvu Mulungu, mwa miyala iyi, kuukitsira Abrahamu ana.
komatu kuyambira kwa iwo a mu Damasiko, ndi a mu Yerusalemu, ndi m'dziko lonse la Yudeya, ndi kwa amitundunso ndinalalikira kuti alape, natembenukire kwa Mulungu, ndi kuchita ntchito zoyenera kutembenuka mtima.
pakuti kale munali mdima, koma tsopano muli kuunika mwa Ambuye; yendani monga ana a kuunika,
odzala nacho chipatso cha chilungamo, chimene chili mwa Yesu Khristu, kuchitira Mulungu ulemerero ndi chiyamiko.