Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Mateyu 22:9 - Buku Lopatulika

Chifukwa chake pitani inu kumphambano za njira, ndipo aliyense amene mukampeze, itanani kuukwatiku.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Chifukwa chake pitani inu kumphambano za njira, ndipo amene aliyense mukampeze, itanani kuukwatiku.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Pitani tsono ku mphambano za miseu, mukaitane aliyense amene mukampeze, kuti abwere kuno ku phwando laukwati.’

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Pitani ku mphambano za misewu ndipo kayitaneni aliyense amene mukamupeze kuti abwere ku phwando.’

Onani mutuwo



Mateyu 22:9
16 Mawu Ofanana  

Pakuti mfumu ya ku Babiloni aima pa mphambano ya njira, polekana njira ziwirizo, kuti aombeze maula; agwedeza mivi, afunsira kwa aterafi, apenda ndi chiwindi.


Ndipo usaime pamphambano kuononga opulumuka ake; kapena kupereka otsala ake tsiku lakupsinjika.


Iwo ananena kwa iye, Chifukwa palibe munthu anatilemba. Iye anati kwa iwo, Pitani inunso kumundawo wampesa.


Ndipo akapolo ao anatulukira kunjira, nasonkhanitsa onse amene anawapeza, ngakhale oipa, ngakhale abwino; ndipo ukwatiwo unadzala ndi okhala pachakudya.


Pomwepo inanena kwa akapolo ake, Za ukwati tsopano zapsa, koma oitanidwawo sanayenere.


ndi kuti kulalikidwe m'dzina lake kulapa ndi kukhululukidwa kwa machimo kwa mitundu yonse, kuyambira ku Yerusalemu.


Pakuti kotero anatilamula Ambuye ndi kuti, Ndakuika iwe kuunika kwa amitundu, kuti udzakhala iwe chipulumutso kufikira malekezero a dziko.


Kwa ine wochepa ndi wochepetsa wa onse oyera mtima anandipatsa chisomo ichi ndilalikire kwa amitundu chuma chosalondoleka cha Khristu;


Ndipo Mzimu ndi mkwatibwi anena, Idzani. Ndipo wakumva anene, Idzani. Ndipo wakumva ludzu adze; iye wofuna, atenge madzi a moyo kwaulere.