Mateyu 22:6 - Buku Lopatulika ndipo otsala anagwira akapolo ake, nawachitira chipongwe, nawapha. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndipo otsala anagwira akapolo ake, nawachitira chipongwe, nawapha. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Enawo adagwira antchito a mfumu aja naŵazunza, nkuŵapha. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo otsalawo anagwira antchito ake, nawazunza ndi kuwapha. |
Koma mfumu inakwiya; nituma asilikali ake napululutsa ambanda aja, nitentha mzinda wao.
Pakuti adzampereka kwa amitundu, nadzamseka, nadzamchitira chipongwe, nadzamthira malovu;
Ndipo Saulo analikuvomerezana nao pa imfa yake. Ndipo tsikulo kunayamba kuzunza kwakukulu pa Mpingo unali mu Yerusalemu; ndipo anabalalitsidwa onse m'maiko a Yudeya ndi Samariya, koma osati atumwi ai.
Kumbukirani am'nsinga, monga am'nsinga anzao; ochitidwa zoipa, monga ngati inunso adatero nanu m'thupi.