Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Mateyu 2:8 - Buku Lopatulika

Nawatumiza ku Betelehemu, nati, Yendani mufunitsitse za kamwanako; ndipo pamene mudzampeza, mundibwezere mau, kuti inenso ndidzadze kudzamlambira Iye.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Nawatumiza ku Betelehemu, nati, Yendani mufunitsitse za kamwanako; ndipo pamene mudzampeza, mundibwezere mau, kuti inenso ndidzadze kudzamlambira Iye.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Kenaka adaŵatumiza ku Betelehemu nkuŵauza kuti, “Pitani, kafunsitseni za mwanayo. Mukakampeza, mudzandidziŵitse, kuti inenso ndidzapite kukampembedza.”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ndipo anawatumiza ku Betelehemu nawawuza kuti, “Pitani mukafufuze za mwanayo mosamalitsa. Ndipo mukamupeza mudzandiwuze kuti inenso ndikamupembedze.”

Onani mutuwo



Mateyu 2:8
20 Mawu Ofanana  

Ndipo Abisalomu ndi anthu onse a Israele anati, Uphungu wa Husai Mwariki uposa uphungu wa Ahitofele. Pakuti kunaikidwa ndi Yehova kutsutsa uphungu wabwino wa Ahitofele kuti Yehova akamtengere Abisalomu choipa.


Tsono Yezebele anatuma mthenga kwa Eliya, wakuti, Milungu indilange nionjezepo, ngati sindilinganiza moyo wako ndi moyo wa mmodzi wa iwowo mawa nthawi yomwe ino.


Kulibe nzeru ngakhale luntha ngakhale uphungu wotsutsana ndi Yehova.


Ndani anganene, chonena chake ndi kuchitikadi, ngati Ambuye salamulira?


Ndipo pa kubadwa kwake kwa Yesu mu Betelehemu wa Yudeya m'masiku a Herode mfumu, onani, Anzeru a kum'mawa anafika ku Yerusalemu,


Pomwepo Herode anawaitana Anzeruwo m'tseri, nafunsitsa iwo nthawi yake idaoneka nyenyeziyo.


Ndipo iwo, m'mene anamva mfumu, anamuka; ndipo onani, nyenyezi ija anaiona kum'mawa, inawatsogolera iwo, kufikira inadza nkuima pamwamba pomwe panali kamwanako.