Mateyu 2:21 - Buku Lopatulika Ndipo anauka iye, natenga kamwana ndi amake, nalowa m'dziko la Israele. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anauka iye, natenga kamwana ndi amake, nalowa m'dziko la Israele. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo Yosefe adanyamuka, nkutenga mwana uja ndi mai wake, kubwerera ku Israele. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono Yosefe atadzuka anatenga mwanayo ndi amayi ake kupita ku dziko la Israeli. |
nati, Tauka, nutenge kamwana ndi amake, nupite kudziko la Israele: chifukwa anafa uja wofuna moyo wake wa kamwanako.
Koma pakumva iye kuti Arkelao anali mfumu ya Yudeya m'malo mwa atate wake Herode, anachita mantha kupita kumeneko; ndipo pamene anachenjezedwa ndi Mulungu m'kulota, anamuka nalowa kudziko la Galileya,
Ndi chikhulupiriro Abrahamu, poitanidwa, anamvera kutuluka kunka kumalo amene adzalandira ngati cholowa; ndipo anatuluka wosadziwa kumene akamukako.