Ndipo Iye anawauzira zinthu zambiri m'mafanizo, nanena, Onani, wofesa anatuluka kukafesa mbeu.
Mateyu 13:53 - Buku Lopatulika Ndipo panali, pamene Yesu anatha mafanizo awa, anachokera kumeneko. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo panali, pamene Yesu anatha mafanizo awa, anachokera kumeneko. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu atatsiriza kunena mafanizoŵa, adachoka kumeneko. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yesu atatsiriza mafanizowa anachoka kumeneko. |
Ndipo Iye anawauzira zinthu zambiri m'mafanizo, nanena, Onani, wofesa anatuluka kukafesa mbeu.
Ndipo Iye anati kwa iwo, Chifukwa chake, mlembi aliyense, wophunzitsidwa mu Ufumu wa Kumwamba, ali wofanana ndi munthu mwini banja, amene atulutsa m'chuma chake zinthu zakale ndi zatsopano.
Ndipo panakhala pamene Yesu anatha mau amenewa, makamu a anthu anazizwa ndi chiphunzitso chake: