Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 13:52 - Buku Lopatulika

52 Ndipo Iye anati kwa iwo, Chifukwa chake, mlembi aliyense, wophunzitsidwa mu Ufumu wa Kumwamba, ali wofanana ndi munthu mwini banja, amene atulutsa m'chuma chake zinthu zakale ndi zatsopano.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

52 Ndipo Iye anati kwa iwo, Chifukwa chake, mlembi aliyense, wophunzitsidwa mu Ufumu wa Kumwamba, ali wofanana ndi munthu mwini banja, amene atulutsa m'chuma chake zinthu zakale ndi zatsopano.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

52 Apo Iye adaŵauza kuti, “Nchifukwa chaketu mphunzitsi aliyense wa Malamulo, amene adaphunzira za Ufumu wakumwamba, ali ngati mwinibanja amene amatulutsa zinthu zatsopano ndi zinthu zakale m'nkhokwe ya chuma chake.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

52 Iye anawawuza kuti, “Chifukwa chake mphunzitsi aliyense wa malamulo amene walangizidwa za ufumu wakumwamba ali ngati mwini nyumba amene amatulutsa chuma chatsopano komanso chakale.”

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 13:52
31 Mawu Ofanana  

Pakuti Ezara adaikiratu mtima wake kuchifuna chilamulo cha Yehova, ndi kuchichita, ndi kuphunzitsa mu Israele malemba ndi maweruzo.


Ndipo ine Arita-kisereksesi, mfumu ine, ndilamulira osunga chuma onse okhala tsidya lija la mtsinjewo, kuti chilichonse akupemphani Ezara wansembe, mlembi wa lamulo la Mulungu wa Kumwamba, chichitike mofulumira;


Ezara amene anakwera kuchokera ku Babiloni, ndiye mlembi waluntha m'chilamulo cha Mose, chimene Yehova Mulungu wa Israele adachipereka; ndipo mfumu inampatsa chopempha iye chonse, monga linamkhalira dzanja la Yehova Mulungu wake.


Chipatso cha wolungama ndi mtengo wa moyo; ndipo wokola mtima ali wanzeru.


Milomo ya anzeru iwanditsa nzeru, koma mtima wa opusa suli wolungama.


Mau a m'kamwa mwa munthu ndiwo madzi akuya; kasupe wa nzeru ndiye mtsinje wodzala.


Mankhwala a chikondi anunkhira, ndi pamakomo pathu zipatso zabwino, za mitundumitundu, zakale ndi zatsopano, zimene ndakukundikira iwe, wokondedwa wanga.


Munthu wabwino atulutsa zabwino m'chuma chake chabwino, ndi munthu woipa atulutsa zoipa m'chuma chake choipa.


Mwamvetsa zonsezi kodi? Iwo anati kwa Iye, Inde.


Ndipo panali, pamene Yesu anatha mafanizo awa, anachokera kumeneko.


Chifukwa cha icho, onani, ndituma kwa inu aneneri ndi anzeru ndi alembi; ena a iwo mudzawapha, mudzawapachika; ndi ena a iwo mudzawakwapula m'masunagoge mwanu, ndi kuwazunza, kuchokera kumudzi umodzi, kufikira kumudzi wina;


Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m'dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera:


Mwa ichinso nzeru ya Mulungu inati, Ndidzatumiza kwa iwo aneneri ndi atumwi; ndipo ena a iwo adzawapha, nadzawazunza;


Ndikupatsani inu lamulo latsopano, kuti mukondane wina ndi mnzake; monga ndakonda inu, kuti inunso mukondane wina ndi mnzake.


monga akumva chisoni, koma akukondwera nthawi zonse; monga aumphawi, koma akulemeretsa ambiri; monga okhala opanda kanthu, ndipo akhala nazo zinthu zonse.


chimene mukhoza kuzindikira nacho, pakuchiwerenga, chidziwitso changa m'chinsinsi cha Khristu,


Kwa ine wochepa ndi wochepetsa wa onse oyera mtima anandipatsa chisomo ichi ndilalikire kwa amitundu chuma chosalondoleka cha Khristu;


monga momwe munaphunzira kwa Epafra kapolo mnzathu wokondedwa, ndiye mtumiki wokhulupirika wa Khristu chifukwa cha ife;


Mau a Khristu akhalitse mwa inu chichulukire mu nzeru yonse, ndi kuphunzitsa ndi kuyambirirana eni okha ndi masalimo, ndi mayamiko ndi nyimbo zauzimu, ndi kuimbira Mulungu ndi chisomo mumtima mwanu.


Asakhale wophunza, kuti podzitukumula ungamgwere mlandu wa mdierekezi.


wogwira mau okhulupirika monga mwa chiphunzitso, kuti akakhoze kuchenjeza m'chiphunzitso cholamitsa, ndi kutsutsa otsutsana naye.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa