Koma kodi nzoona kuti Mulungu akhala ndi anthu padziko lapansi? Taonani, thambo, inde m'mwambamwamba, sizifikira inu, koposa kotani nanga nyumba iyi ndaimanga?
Mateyu 12:6 - Buku Lopatulika Koma ndinena kwa inu, kuti wakuposa Kachisiyo ali pompano. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma ndinena kwa inu, kuti wakuposa Kachisiyo ali pompano. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipotu ndikunenetsa kuti pali wina pano woposa Nyumba ya Mulunguyo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ine ndikuwuzani kuti wamkulu kuposa Nyumba ya Mulunguyo ali pano. |
Koma kodi nzoona kuti Mulungu akhala ndi anthu padziko lapansi? Taonani, thambo, inde m'mwambamwamba, sizifikira inu, koposa kotani nanga nyumba iyi ndaimanga?
Atero Yehova, Kumwamba ndi mpando wanga wachifumu, ndi dziko lapansi ndi choikapo mapazi anga; mudzandimangira Ine nyumba yotani? Ndi malo ondiyenera kupumamo ali kuti?
Pakuti zonsezi mkono wanga wazilenga, momwemo zonsezi zinaoneka, ati Yehova; koma ndidzayang'anira munthu uyu amene ali waumphawi, ndi wa mzimu wosweka, nanthunthumira ndi mau anga.
Taonani, ndituma mthenga wanga, kuti akonzeretu njira pamaso panga; ndipo Ambuye amene mumfuna adzadza ku Kachisi wake modzidzimutsa; ndiye mthenga wa chipangano amene mukondwera naye; taonani akudza, ati Yehova wa makamu.
Kapena simunawerenge kodi m'chilamulo, kuti tsiku la Sabata ansembe mu Kachisi amaipitsa tsiku la Sabata, nakhala opanda tchimo?