Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Mateyu 1:17 - Buku Lopatulika

Motero mibadwo yonse kuyambira pa Abrahamu kufikira kwa Davide ndiyo mibadwo khumi ndi inai; ndi kuyambira pa Davide kufikira pa kutengedwa kunka ku Babiloni mibadwo khumi ndi inai; ndi kuyambira pa kutengedwa kunka ku Babiloni kufikira kwa Khristu mibadwo khumi ndi inai.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Motero mibadwo yonse kuyambira pa Abrahamu kufikira kwa Davide ndiyo mibadwo khumi ndi inai; ndi kuyambira pa Davide kufikira pa kutengedwa kunka ku Babiloni mibadwo khumi ndi inai; ndi kuyambira pa kutengedwa kunka ku Babiloni kufikira kwa Khristu mibadwo khumi ndi inai.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Choncho panali mibadwo khumi ndi inai kuyambira pa Abrahamu mpaka pa mfumu Davide, mibadwo khumi ndi inai kuyambira pa Davideyo mpaka pa nthaŵi imene Aisraele adaatengedwa ukapolo kupita ku Babiloni, ndiponso mibadwo khumi ndi inai kuyambira pa nthaŵi yotengedwa ukapolo kupita ku Babiloni mpaka pa nthaŵi ya Khristu, Mpulumutsi wolonjezedwa uja.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Kuyambira pa Abrahamu mpaka pa Davide, pali mibado khumi ndi inayi. Ndipo kuyambira pa Davide mpaka pamene Ayuda anatengedwa kupita ku ukapolo ku Babuloni, pali mibado khumi ndi inayi. Ndiponso kuyambira nthawi ya ukapolo ku Babuloni mpaka pamene Khristu anabadwa, palinso mibado khumi ndi inayi.

Onani mutuwo



Mateyu 1:17
5 Mawu Ofanana  

Nachoka nao a mu Yerusalemu onse, ndi akalonga onse, ndi ngwazi zonse, ndiwo andende zikwi khumi, ndi amisiri onse, ndi osula onse; sanatsale ndi mmodzi yense, koma anthu osauka okhaokha a m'dziko.


zimene sanazitenge Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, pamene anamtenga ndende Yekoniya mwana wake wa Yehoyakimu, mfumu ya Yuda, kuchokera ku Yerusalemu kunka ku Babiloni; ndi akulu onse a Yuda ndi Yerusalemu;


Koma Yohane, pakumva m'nyumba yandende ntchito za Khristu, anatumiza ophunzira ake mau,


Anayamba iye kupeza mbale wake yekha Simoni, nanena naye, Tapeza ife Mesiya (ndiko kusandulika Khristu).