Woyamba ndipo anabala mwana wamwamuna, namtcha dzina lake. Mowabu; yemweyo ndi atate wa Amowabu kufikira lero.
Masalimo 83:9 - Buku Lopatulika Muwachitire monga munachitira Midiyani; ndi Sisera, ndi Yabini kumtsinje wa Kisoni, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Muwachitire monga munachitira Midiyani; ndi Sisera, ndi Yabini kumtsinje wa Kisoni, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Muŵachite zomwe mudaŵachita Amidiyani, Sisera ndi Yabini ku mtsinje wa Kisoni, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Muwachitire zomwe munachitira Amidiyani, monga munachitira Sisera ndi Yabini ku mtsinje wa Kisoni. |
Woyamba ndipo anabala mwana wamwamuna, namtcha dzina lake. Mowabu; yemweyo ndi atate wa Amowabu kufikira lero.
Wamng'ono ndipo anabala mwana wamwamuna, namtcha dzina lake Benami; yemweyo ndi atate wa Aamoni kufikira lero.
Ndipo Yehova wa makamu adzamuutsira chikoti, monga m'kuphedwa kwa Midiyani pa thanthwe la Orebu; ndipo chibonga chake chidzakhala pamwamba pa nyanja, ndipo adzaisamula monga anachitira Ejipito,
Pakuti goli la katundu wake, ndi mkunkhu wa paphewa pake, ndodo ya womsautsa, inu mwazithyola monga tsiku la Midiyani.
Ndipo ndidzamkoka Sisera, kazembe wa nkhondo ya Yabini, akudzere ku mtsinje wa Kisoni, ndi magaleta ake, ndi aunyinji ake; ndipo ndidzampereka m'dzanja lako.
Mtsinje wa Kisoni unawakokolola, mtsinje uja wakale, mtsinje wa Kisoni. Yenda mwamphamvu, moyo wangawe.