Masalimo 17:2 - Buku Lopatulika Pankhope panu patuluke chiweruzo changa; maso anu apenyerere zolunjika. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pankhope panu patuluke chiweruzo changa; maso anu apenyerere zolunjika. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kusalakwa kwanga kuwonekere poyera pa chiweruzo chanu, maso anu aone kulungama kwanga. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kusalakwa kwanga kuchokera kwa inu; maso anu aone chimene ndi cholungama. |
Koma mukuti, Njira ya Ambuye njosayenera. Tamvera tsono nyumba ya Israele, Kodi njira yanga njosayenera? Njira zanu si ndizo zosayenera?
Koma nyumba ya Israele imanena, Njira ya Ambuye njosayenera. Inu, nyumba ya Israele, kodi njira zanga nzosayenera? Njira zanu si ndizo zosayenera?
Koma ana a anthu a mtundu wako akuti, Njira ya Ambuye siiyenera; koma iwowa njira yao siiyenera.
Koma munati, Njira ya Ambuye siiyenera. Nyumba ya Israele inu, ndidzakuweruzani, yense monga mwa njira zake.
Ndipo kwa Iye amene akhoza kukudikirani mungakhumudwe, ndi kukuimikani pamaso pa ulemerero wake opanda chilema m'kukondwera,