Masalimo 139:4 - Buku Lopatulika Pakuti asanafike mau pa lilime langa, taonani, Yehova, muwadziwa onse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti asanafike mau pa lilime langa, taonani, Yehova, muwadziwa onse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ngakhale mau anga asanafike pakamwa panga, Inu Chauta mumaŵadziŵa onse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mawu asanatuluke pa lilime langa mumawadziwa bwinobwino, Inu Yehova. |
Ndani uyu abisa uphungu wosadziwa kanthu? Chifukwa chake ndinafotokozera zimene sindinazizindikire, zondidabwitsa, zosazidziwa ine.
Udzanena izi kufikira liti? Ndipo mau a pakamwa pako adzakhala ngati namondwe kufikira liti?
Mau a m'kamwa mwanga ndi maganizo a m'mtima wanga avomerezeke pamaso panu, Yehova, thanthwe langa, ndi Mombolo wanga.
chifukwa anachita zopusa mu Israele, nachita chigololo ndi akazi a anansi ao, nanena mau onama m'dzina langa, amene ndinawauza kuti asanene; Ine ndine wodziwa, ndi mboni, ati Yehova.
Ndipo kudzachitika nthawi yomweyi kuti ndidzasanthula Yerusalemu ndi nyali, ndipo ndidzalanga amunawo okhala ndi nsenga, onena m'mtima mwao, Yehova sachita chokoma, kapena kuchita choipa.
Ngati wina adziyesera ali wopembedza Mulungu, ndiye wosamanga lilime lake, koma adzinyenga mtima wake, kupembedza kwake kwa munthuyu nkopanda pake.