Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Marko 4:5 - Buku Lopatulika

Ndipo zina zinagwa pa nthaka yathanthwe, pamene panalibe nthaka yambiri; ndipo pomwepo zinamera, chifukwa zinalibe nthaka yakuya;

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo zina zinagwa pa nthaka yathanthwe, pamene panalibe nthaka yambiri; ndipo pomwepo zinamera, chifukwa zinalibe nthaka yakuya;

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mbeu zina zidagwera pa nthaka yamiyala, pamene panalibe dothi lambiri. Zidamera msanga, chifukwa nthakayo inali yosazama.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Zina zinagwa pa malo a miyala pamene panalibe dothi lambiri. Zinamera mofulumira chifukwa panalibe dothi lambiri.

Onani mutuwo



Marko 4:5
11 Mawu Ofanana  

Ndipo ndidzawapatsa mtima umodzi, ndi kuika mzimu watsopano m'kati mwao; ndipo ndidzawachotsera mtima wamwala m'thupi mwao, ndi kuwapatsa mtima wamnofu;


Ndipo ndidzakupatsani mtima watsopano, ndi kulonga m'kati mwanu mzimu watsopano; ndipo ndidzachotsa mtima wamwala m'thupi, ndi kukupatsani mtima wamnofu.


Mudzibzalire m'chilungamo mukolole monga mwa chifundo; limani masala anu, pakuti yafika nthawi ya kufuna Yehova, mpaka afika Iye, navumbitsira inu chilungamo.


Kodi akavalo adzathamanga pathanthwe? Kodi adzalimako ndi ng'ombe pakuti mwasanduliza chiweruzo chikhale ndulu, ndi chipatso cha chilungamo chikhale chivumulo;


Koma iye amene afesedwa pamiyala, uyu ndiye wakumva mau, ndi kuwalandira pomwepo ndi kusekera;


ndipo kunali, m'kufesa kwake, zina zinagwa m'mbali mwa njira, ndi mbalame zinadza ndi kuzitha kudya.


ndipo litakwera dzuwa zinapserera; ndipo popeza zinalibe mizu zinakhwinyata.


Ndipo za pathanthwe ndiwo amene, pakumva, alandira mau ndi kukondwera; koma alibe mizu; akhulupirira kanthawi, ndipo pa nthawi ya mayesedwe angopatuka.


Ndipo zina zinagwa pathanthwe; ndipo pakumera zinatofa msanga, chifukwa zinalibe mnyontho.