Kuchilamulo ndi kuumboni! Ngati iwo sanena malinga ndi mau awa, ndithu sadzaona mbandakucha.
Marko 10:3 - Buku Lopatulika Ndipo Iye anayankha nati kwa iwo, Kodi Mose anakulamulani chiyani? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Iye anayankha nati kwa iwo, Kodi Mose anakulamulani chiyani? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma Yesu poyankha adati, “Kodi Mose adakulamulani zotani?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anayankha kuti, “Kodi Mose anakulamulani chiyani?” |
Kuchilamulo ndi kuumboni! Ngati iwo sanena malinga ndi mau awa, ndithu sadzaona mbandakucha.
Ndipo anadza kwa Iye Afarisi, namfunsa Iye ngati kuloledwa kuti munthu achotse mkazi wake, namuyesa Iye.
Ndipo taonani, wachilamulo wina anaimirira namuyesa Iye, nanena, Mphunzitsi, ndidzalowa moyo wosatha ndi kuchita chiyani?
Musanthula m'malembo, popeza muyesa kuti momwemo muli nao moyo wosatha; ndipo akundichitira Ine umboni ndi iwo omwewo;