Taona Mtumiki wanga, amene ndimgwiriziza; Wosankhika wanga, amene moyo wanga ukondwera naye; ndaika mzimu wanga pa Iye; Iye adzatulutsira amitundu chiweruziro.
Marko 1:10 - Buku Lopatulika Ndipo pomwepo, alimkukwera potuluka m'madzi, anaona Iye thambo litang'ambika, ndi Mzimu alikutsikira pa Iye monga nkhunda: Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pomwepo, alimkukwera potuluka m'madzi, anaona Iye thambo litang'ambika, ndi Mzimu alikutsikira pa Iye monga nkhunda: Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Potuluka m'madzimo, adangoona kuthambo kukutsekuka, ndipo Mzimu Woyera akutsika pa Iye ngati nkhunda. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamene Yesu ankatuluka mʼmadzi, anaona kumwamba kukutsekuka ndipo Mzimu Woyera akutsikira pa Iye ngati nkhunda. |
Taona Mtumiki wanga, amene ndimgwiriziza; Wosankhika wanga, amene moyo wanga ukondwera naye; ndaika mzimu wanga pa Iye; Iye adzatulutsira amitundu chiweruziro.
Ndipo kunali chaka cha makumi atatu, mwezi wachinai, tsiku lachisanu la mwezi, pokhala ine pakati pa andende kumtsinje Kebara, kunatseguka kumwamba, ndipo ndinaona masomphenya a Mulungu.
Ndipo Yesu, pamene anabatizidwa, pomwepo anatuluka m'madzi: ndipo onani, miyamba inamtsegukira Iye, ndipo anapenya Mzimu wa Mulungu wakutsika ngati nkhunda nudza nutera pa Iye;
Ndipo kunali masiku omwewo, Yesu anadza kuchokera ku Nazarete wa ku Galileya, nabatizidwa ndi Yohane mu Yordani.
ndipo Mzimu Woyera anatsika ndi maonekedwe a thupi lake ngati nkhunda, nadza pa Iye; ndipo munatuluka mau m'thambo, kuti, Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa, mwa Iwe ndikondwera.