Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 3:22 - Buku Lopatulika

22 ndipo Mzimu Woyera anatsika ndi maonekedwe a thupi lake ngati nkhunda, nadza pa Iye; ndipo munatuluka mau m'thambo, kuti, Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa, mwa Iwe ndikondwera.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 ndipo Mzimu Woyera anatsika ndi maonekedwe a thupi lake ngati nkhunda, nadza pa Iye; ndipo munatuluka mau m'thambo, kuti, Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa, mwa Iwe ndikondwera.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 ndipo Mzimu Woyera adatsikira pa Iye, akuwoneka ndi thupi ngati la nkhunda. Tsono kudamveka mau ochokera Kumwamba akuti, “Iwe ndiwe Mwana wanga wapamtima. Ndimakondwera nawe kwambiri.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Mzimu Woyera anatsika pa Iye mumaonekedwe a nkhunda ndipo mawu anamveka kuchokera kumwamba: “Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa; ndimakondwera nawe.”

Onani mutuwo Koperani




Luka 3:22
21 Mawu Ofanana  

Ndidzauza za chitsimikizo: Yehova ananena ndi Ine, Iwe ndiwe Mwana wanga; Ine lero ndakubala.


Taona Mtumiki wanga, amene ndimgwiriziza; Wosankhika wanga, amene moyo wanga ukondwera naye; ndaika mzimu wanga pa Iye; Iye adzatulutsira amitundu chiweruziro.


Taona mnyamata wanga, amene ndinamsankha, wokondedwa wanga, amene moyo wanga ukondwera naye; pa Iye ndidzaika Mzimu wanga, ndipo Iye adzalalikira chiweruzo kwa akunja.


Akali chilankhulire, onani, mtambo wowala unawaphimba iwo: ndipo onani, mau ali kunena mumtambo, Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa iyeyu ndikondwera, mverani Iye.


Amakhulupirira Mulungu; Iye ampulumutse tsopano, ngati amfuna; pakuti anati, Ine ndine Mwana wa Mulungu.


Pamenepo Yesu anachokera ku Galileya nadza ku Yordani kwa Yohane, kudzabatizidwa ndi iye.


Ndipo Yesu, pamene anabatizidwa, pomwepo anatuluka m'madzi: ndipo onani, miyamba inamtsegukira Iye, ndipo anapenya Mzimu wa Mulungu wakutsika ngati nkhunda nudza nutera pa Iye;


ndipo onani, mau akuchokera kumiyamba akuti, Uyu ndiye mwana wanga wokondedwa, mwa Iyeyu ndikondwera.


ndipo mau anatuluka m'thambo, Mwana wanga wokondedwa ndiwe, mwa Iwe ndikondwera bwino.


Ndipo kunali masiku omwewo, Yesu anadza kuchokera ku Nazarete wa ku Galileya, nabatizidwa ndi Yohane mu Yordani.


Ndipo panadza mtambo wakuwaphimba iwo; ndipo mau munatuluka m'mtambomo, kuti, Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa; mverani Iye.


Ulemerero ukhale kwa Mulungu Kumwambamwamba, ndi mtendere pansi pano mwa anthu amene akondwera nao.


Ndipo anayamba kunena kwa iwo, kuti, Lero lembo ili lakwanitsidwa m'makutu anu.


Ndipo Yohane anachita umboni, nati, Ndinaona Mzimu alikutsika kuchokera Kumwamba monga nkhunda; nakhalabe pa Iye.


Atate, lemekezani dzina lanu. Pomwepo adadza mau ochokera Kumwamba, Ndalilemekeza, ndipo ndidzalilemekezanso.


Ndipo Atate wonditumayo, Iyeyu wandichitira Ine umboni. Simunamva mau ake konse, kapena maonekedwe ake simunaone.


za Yesu wa ku Nazarete, kuti Mulungu anamdzoza Iye ndi Mzimu Woyera ndi mphamvu; amene anapitapita nachita zabwino, nachiritsa onse osautsidwa ndi mdierekezi, pakuti Mulungu anali pamodzi ndi Iye.


amene anatilanditsa ife kuulamuliro wa mdima, natisunthitsa kutilowetsa mu ufumu wa Mwana wa chikondi chake;


amene pakudza kwa Iye, mwala wamoyo, wokanidwatu ndi anthu, koma ndi Mulungu wosankhika, waulemu,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa