Ndipo m'mzinda uliwonse, kapena m'mudzi, mukalowamo, mufunsitse amene ali woyenera momwemo; ndipo bakhalani komweko kufikira mutulukamo.
Luka 9:4 - Buku Lopatulika Ndipo m'nyumba iliyonse mukalowemo, khalani komweko, ndipo muzikachokera kumeneko. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo m'nyumba iliyonse mukalowemo, khalani komweko, ndipo muzikachokera kumeneko. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo mukafikira kunyumba kwina, mukhale nao kumeneko mpaka itakwana nthaŵi yoti muchoke kumudziko. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nyumba iliyonse imene mulowa, mukhale momwemo kufikira mutachoka mu mzindawo. |
Ndipo m'mzinda uliwonse, kapena m'mudzi, mukalowamo, mufunsitse amene ali woyenera momwemo; ndipo bakhalani komweko kufikira mutulukamo.
Ndipo ananena nao, Kumene kulikonse mukalowa m'nyumba, khalani komweko kufikira mukachokako.
Ndipo Iye anati kwa iwo, Musanyamule kanthu ka paulendo, kapena ndodo, kapena thumba, kapena mkate, kapena ndalama; ndipo musakhale nao malaya awiri.
Ndipo onse amene sakakulandireni inu, m'mene mutuluka m'mudzi womwewo, sansani fumbi la pa mapazi anu, likhale mboni ya paiwo.
Pamene anabatizidwa iye ndi a pabanja pake anatidandaulira ife, kuti, Ngati mwandiyesera ine wokhulupirika kwa Ambuye, mulowe m'nyumba yanga, mugone m'menemo. Ndipo anatiumiriza ife.