Yehova Inu, maso anu sali pachoonadi kodi? Munawapanda iwo, koma sanaphwetekedwe mtima; munawatha iwo, koma akana kudzudzulidwa; alimbitsa nkhope zao koposa mwala; akana kubwera.
Luka 8:6 - Buku Lopatulika Ndipo zina zinagwa pathanthwe; ndipo pakumera zinatofa msanga, chifukwa zinalibe mnyontho. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo zina zinagwa pathanthwe; ndipo pakumera zinatofa msanga, chifukwa zinalibe mnyontho. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mbeu zina zidagwera pa nthaka yapathanthwe. Zidamera, koma nkufota, chifukwa zidaasoŵa chinyontho. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Zina zinagwa pa thanthwe, ndipo pamene zinamera, zinafota chifukwa panalibe chinyezi. |
Yehova Inu, maso anu sali pachoonadi kodi? Munawapanda iwo, koma sanaphwetekedwe mtima; munawatha iwo, koma akana kudzudzulidwa; alimbitsa nkhope zao koposa mwala; akana kubwera.
Ndipo ndidzawapatsa mtima umodzi, ndi kuika mzimu watsopano m'kati mwao; ndipo ndidzawachotsera mtima wamwala m'thupi mwao, ndi kuwapatsa mtima wamnofu;
Ndipo ndidzakupatsani mtima watsopano, ndi kulonga m'kati mwanu mzimu watsopano; ndipo ndidzachotsa mtima wamwala m'thupi, ndi kukupatsani mtima wamnofu.
Kodi akavalo adzathamanga pathanthwe? Kodi adzalimako ndi ng'ombe pakuti mwasanduliza chiweruzo chikhale ndulu, ndi chipatso cha chilungamo chikhale chivumulo;
Ndipo za pathanthwe ndiwo amene, pakumva, alandira mau ndi kukondwera; koma alibe mizu; akhulupirira kanthawi, ndipo pa nthawi ya mayesedwe angopatuka.
Anatuluka wofesa kukafesa mbeu zake; ndipo m'kufesa kwake zina zinagwa m'mbali mwa njira; ndipo zinapondedwa, ndi mbalame za m'mlengalenga zinatha kuzidya.
umo anenamo, Lero ngati mudzamva mau ake, musaumitse mitima yanu, monga pa kupsetsa mtima.