Chigwa chilichonse chidzadzazidwa, ndipo phiri lililonse ndi chitunda chilichonse zidzachepetsedwa, ndipo zokhota zidzaongoledwa, ndipo zamakolokoto zidzasalala;
Luka 3:5 - Buku Lopatulika Chigwa chilichonse chidzadzazidwa, ndipo phiri lililonse ndi mtunda uliwonse zidzachepsedwa; ndipo zokhota zidzakhala zolungama, ndipo njira za zigoloondo zidzakhala zosalala; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chigwa chilichonse chidzadzazidwa, ndipo phiri lililonse ndi mtunda uliwonse zidzachepsedwa; ndipo zokhota zidzakhala zolungama, ndipo njira za zigoloondo zidzakhala zosalala; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Dzazani chigwa chilichonse, chepetsani phiri lililonse ndi mtunda uliwonse. Ongolani njira zokhotakhota, salazani njira zazigolowondo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Chigwa chilichonse chidzadzazidwa ndipo phiri lililonse ndi mtunda uliwonse zidzasalazidwa, misewu yokhotakhota idzawongoledwa, ndi njira zosasalala zidzasalazidwa. |
Chigwa chilichonse chidzadzazidwa, ndipo phiri lililonse ndi chitunda chilichonse zidzachepetsedwa, ndipo zokhota zidzaongoledwa, ndipo zamakolokoto zidzasalala;
Ndipo ndidzayendetsa akhungu m'khwalala, limene iwo salidziwa, m'njira zimene iwo sazidziwa ndidzawatsogolera; ndidzawalitsa mdima m'tsogolo mwao, ndi kulungamitsa malo okhota. Zinthu izi Ine ndidzachita, ndipo sindidzawasiya.
Ndidzakutsogolera ndi kusalaza pokakala; ndidzathyolathyola zitseko zamkuwa, ndi kudula pakati akapichi achitsulo;
Ndipo mitengo yonse yakuthengo idzadziwa kuti Ine Yehova ndatsitsa mtengo wosomphoka, ndakuza mtengo waung'ono, ndaumitsa mtengo wauwisi, ndi kuphukitsa mtengo wouma; Ine Yehova ndanena ndi kuchichita.