Luka 22:1 - Buku Lopatulika Ndipo chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa chinayandikira, ndicho chotchedwa Paska. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo phwando la mikate yopanda chotupitsa linayandikira, ndilo lotchedwa Paska. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nthaŵi yochitira chikondwerero cha buledi wosafufumitsa inkayandikira. Chikondwererocho chimatchedwa Paska. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Phwando la buledi wopanda yisiti lotchedwa Paska litayandikira, |
Ndipo tsiku loyamba la mikate yopanda chotupitsa, pamene amapha Paska, ophunzira ananena naye, Mufuna tinke kuti, tikakonze mkadyereko Paska?
Koma pasanafike chikondwerero la Paska, Yesu, podziwa kuti nthawi yake idadza yakuchoka kutuluka m'dziko lino lapansi, kunka kwa Atate, m'mene anakonda ake a Iye yekha a m'dziko lapansi, anawakonda kufikira chimaliziro.