Ndipo anadza mkazi wamasiye waumphawi, ndipo iye anaponyamo tindalama tiwiri tating'ono tokwanira kakobiri kamodzi.
Luka 21:2 - Buku Lopatulika Ndipo anaona mkazi wina wamasiye waumphawi alikuika momwemo timakobiri tiwiri. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anaona mkazi wina wamasiye waumphawi alikuika momwemo timakobiri tiwiri. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adaonanso mai wina wamasiye akuponyamo tindalama tiŵiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anaonanso mkazi wamasiye wosauka akuyikamo timakopala tiwiri. |
Ndipo anadza mkazi wamasiye waumphawi, ndipo iye anaponyamo tindalama tiwiri tating'ono tokwanira kakobiri kamodzi.