Chiweruzo cha Yehova chikhazikika chikhazikikire, zolingirira za m'mtima mwake ku mibadwomibadwo.
Luka 2:6 - Buku Lopatulika Ndipo panali pokhala iwo komweko, masiku ake a kubala anakwanira. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo panali pokhala iwo komweko, masiku ake a kubala anakwanira. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamene anali kumeneko, nthaŵi yake yoti Maria achire idakwana, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ali kumeneko, nthawi inakwana yakuti mwana abadwe, |
Chiweruzo cha Yehova chikhazikika chikhazikikire, zolingirira za m'mtima mwake ku mibadwomibadwo.
Koma iwe, Betelehemu Efurata, ndiwe wamng'ono kuti ukhale mwa zikwi za Yuda, mwa iwe mudzanditulukira wina wakudzakhala woweruza mu Israele; matulukiro ake ndiwo a kale lomwe, kuyambira nthawi yosayamba.
kukalembedwa iye mwini pamodzi ndi Maria, wopalidwa naye ubwenzi; ndi uyu anali ndi pakati.
Ndipo iye anabala mwana wake wamwamuna woyamba; namkulunga Iye m'nsalu, namgoneka modyera ng'ombe, chifukwa kuti anasowa malo m'nyumba ya alendo.