Ndipo mwanayo anakula, nalimbika mu mzimu wake, ndipo iye anali m'mapululu, kufikira masiku akudzionetsa yekha kwa Israele.
Luka 2:52 - Buku Lopatulika Ndipo Yesu anakulabe m'nzeru ndi mumsinkhu, ndi m'chisomo cha pa Mulungu ndi cha pa anthu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yesu anakulabe m'nzeru ndi mumsinkhu, ndi m'chisomo cha pa Mulungu ndi cha pa anthu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo Yesu analikunka nakula m'nzeru ndi mu msinkhu, ndipo Mulungu ndi anthu omwe ankakondwera naye kwambiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Yesu anakula mu nzeru, msinkhu ndi chisomo cha Mulungu ndi anthu. |
Ndipo mwanayo anakula, nalimbika mu mzimu wake, ndipo iye anali m'mapululu, kufikira masiku akudzionetsa yekha kwa Israele.
Ndipo mwanayo anakula nalimbika, nalikudzala ndi nzeru; ndi chisomo cha Mulungu chinali pa Iye.
Pakuti iye amene atumikira Khristu mu izi akondweretsa Mulungu, navomerezeka ndi anthu.