Tonse tasochera ngati nkhosa; tonse tayenda yense m'njira ya mwini yekha; ndipo Yehova anaika pa Iye mphulupulu ya ife tonse.
Luka 15:3 - Buku Lopatulika Koma anati kwa iwo fanizo ili, nanena, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma anati kwa iwo fanizo ili, nanena, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Yesu adaŵaphera fanizo ili, adati, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Yesu anawawuza fanizo ili: |
Tonse tasochera ngati nkhosa; tonse tayenda yense m'njira ya mwini yekha; ndipo Yehova anaika pa Iye mphulupulu ya ife tonse.
Ndipo ndidzasangalala mu Yerusalemu, ndi kukondwera mwa anthu anga; ndipo mau akulira sadzamvekanso mwa iye, pena mau akufuula.
Ndipo Iye anawauzira zinthu zambiri m'mafanizo, nanena, Onani, wofesa anatuluka kukafesa mbeu.
Koma mukani muphunzire nchiyani ichi, Ndifuna chifundo, si nsembe ai; pakuti sindinadze kudzaitana olungama, koma ochimwa.
Munthu ndani wa inu ali nazo nkhosa makumikhumi, ndipo pakutayika imodzi ya izo, sasiya nanga m'chipululu zinazo makumi asanu ndi anai mphambu zisanu ndi zinai, nalondola yotayikayo kufikira aipeza?
Ananena nayenso kachiwiri, Simoni mwana wa Yona, ukonda Ine kodi? Ananena ndi Iye, Inde, Ambuye; mudziwa kuti ndikukondani Inu. Ananena naye, Weta nkhosa zanga.
Ndipo pamene anazimva, analemekeza Mulungu; nati kwa iye, Uona, mbale, kuti ambirimbiri mwa Ayuda akhulupirira; ndipo ali nacho changu onsewa, cha pa chilamulo;