Ndipo Yehova anavumbitsa pa Sodomu ndi pa Gomora miyala ya sulufure ndi moto kutuluka kwa Mulungu kumwamba;
Luka 10:12 - Buku Lopatulika Ndinena ndi inu kuti tsiku lijalo ku Sodomu kudzapiririka kuposa mudzi umenewo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndinena ndi inu kuti tsiku lijalo ku Sodomu kudzapiririka kuposa mudzi umenewo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kunena zoona, pa tsiku lachiweruzo, Mulungu adzachitako chifundo polanga Sodomu koposa polanga mudzi umenewo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ine ndikuwuzani kuti adzachita chifundo polanga Sodomu pa tsikulo kusiyana ndi mudziwo. |
Ndipo Yehova anavumbitsa pa Sodomu ndi pa Gomora miyala ya sulufure ndi moto kutuluka kwa Mulungu kumwamba;
Pakuti mphulupulu ya mwana wamkazi wa anthu a mtundu wanga, ikula koposa tchimo la Sodomu, umene unapasuka m'kamphindi, anthu osauchitira kanthu.
Indetu ndinena kwa inu, kuti, tsiku la kuweruza, mlandu wao wa Sodomu ndi Gomora udzachepa ndi wake wa mudzi umenewo.
Komanso ndinena kwa inu kuti tsiku la kuweruza, mlandu wake wa Sodomu udzachepa ndi wako.
Ndipo pamalo ponse sakulandirani, kapena kumvera inu, pakuchoka kumeneko, sansani fumbi lili kumapazi anu, likhale mboni ya kwa iwo.