kuti ukadziwitse ntheradi yake ya mau oona, nukabwere ndi mau oona kwa iwo amene anakutumiza?
Luka 1:4 - Buku Lopatulika kuti udziwitse zoona zake za mau amene unaphunzira. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 kuti udziwitse zoona zake za mau amene unaphunzira. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndatero kuti mudziŵe ndithu kuti zimene adakuphunzitsanizo nzoonadi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero kuti mudziwe bwinobwino zoona za zinthu zimene mwaphunzitsidwa. |
kuti ukadziwitse ntheradi yake ya mau oona, nukabwere ndi mau oona kwa iwo amene anakutumiza?
koma zalembedwa izi kuti mukakhulupirire kuti Yesu ndiye Khristu Mwana wa Mulungu, ndi kuti pakukhulupirira mukhale nao moyo m'dzina lake.
Iyeyo anaphunzitsidwa m'njira ya Ambuye; pokhala nao mzimu wachangu, ananena ndi kuphunzitsa mosamalira zinthu za Yesu, ndiye wodziwa ubatizo wa Yohane wokha;
koma mu Mpingo ndifuna kulankhula mau asanu ndi zidziwitso changa, kutinso ndikalangize ena, koposa kulankhula mau zikwi m'lilime.